Bishop Charles Kapenga omwe anali mtsogoleri wa mpingo wa Believers Assembly International amwalira.
Malingana ndi malipoti omwe tikutsatira, Bishop Kapenga omwe ndi bambo ake a woyimba wachisodzera Waxy K, atisiya m’bandakucha wa lero Lamulungu ku chipatala cha Queen Elizabeth Central munzinda wa Blantyre.
Iwo atisiya atadwala nthawi yochepa, ndipo pakadali pano dongosolo la mwambo wa maliro silinadziwike.
Mzimu wawo uwuse mumtendere
No comments:
Post a Comment